Psalms 138

Salimo la Davide.

1Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
ndipo ndidzayamika dzina lanu
chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
kupambana zinthu zonse.
3Pamene ndinayitana, munandiyankha;
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

4Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
pamene amva mawu a pakamwa panu.
5Iwo ayimbe za njira za Yehova,
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

6Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
7Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
musasiye ntchito ya manja anu.
Copyright information for NyaCCL